Wikipedia nywiki https://ny.wikipedia.org/wiki/Tsamba_Lalikulu MediaWiki 1.47.0-wmf.24 first-letter Media Special Talk User User talk Wikipedia Wikipedia talk File File talk MediaWiki MediaWiki talk Template Template talk Help Help talk Category Category talk TimedText TimedText talk Module Module talk Event Event talk Malaŵi 0 1401 72039 52864 2026-10-28T09:56:59Z Таёжный лес 11379 /* Maboma a Malawi */ 72039 wikitext text/x-wiki {{Thebulo_dziko | | dzina= {{nowrap|{{lang|ny|Dziko la Malaŵi}}}} ([[Chewa language|Chichewa]])<br>{{nowrap|{{lang|ny|Chalo cha Malaŵi}}}} ([[Tumbuka language|Chitumbuka]]) | mbendera = [[File:Flag of Malawi.svg|125px|Mbendera ya Malaŵi]] | chikopa = [[File:Coat of arms of Malawi.svg|140px|Chikopa cha Malaŵi]] | malo = [[File:LocationMalawi.svg|250px|Malaŵi ku Afrika]] | chinenero = [[Chichewa]] | m'zinda = [[Lilongwe]] | chipembedzo = [[Protestant]]&nbsp;55%, [[Catholic]]&nbsp;20%, [[Muslim]]&nbsp;20% | boma lolamulira = [[Republic]] | km2 = 118,484 | madzi = 20 | wam'dziko = 18.1 million (2016)| density = 153 | ndalama = [[kwacha ya Malaŵi]] | code_ndalama = MAK | nthawi = +1 | nyimbo ya pfuko= [[Mulungu dalitsani Malaŵi]] | Tsiku lopata ufulu= Juli 6 | tld = mw | landcode = MWI | tel = 265 }} [[File:Otter Point, Cape Maclear (Malawi).jpg|thumb|250px|Otter Point, Cape Maclear]] '''Dziko la Malaŵi''' lomwe kale linkatchulidwa kuti [[Nyasaland]], ndi dziko la demokilase lomwe lili ndi anthu ambiri ndipo lili cha ku m’mwera kwa [[Africa]]. Dzikoli linayandikana ndi [[Zambia]] cha ku m'madzulo, [[Tanzania]] cha ku mpoto ndi [[Mozambique]] kuzungulira kum’mawa, kum'mwera ndi ku m'madzulo. Chiyambi cha dzina loti Malawi sichidziwika bwino bwino, koma anthu ofufuza amakhulupilira kuti dzinali linachokela kwa chilankhulo cha anthu a mu dzikoli a ku chigawo cha kum'mwera, ndipo limatanthauza “malawi wa moto”, koma mbendela ya dzikoli limatanthauza "kwacha" kunena kuti dzuwa lawala m'mamawa.[[Purezidenti wa Malawi]] == Mbiri == Anthu oyamba mu dziko la Malawi anali a chi [[Khoisan]], amene ankachita ulenje komanso kutolela zakudya zomera zokha. Anthu a Chibantu anabwera ku dzikoli nthawi wa [[kusamuka kwa anthu a chi Bantu]]. Dziko lomwe limatchulidwa kuti Malawi panoli ndi dera la [[Maravi]], lomwe linakhazikitsidwa ndi anthu a Chichewa mu zaka za ku ma 1600. Achewa anali ochokera ku gulu la anthu lotchedwa ma Luba. Koyambilira ndi pakati pa zaka za mma 1900, anthu a Chizulu ochokela ku Ndandwe, [[KwaZulu-Natal]] mdziko la [[South Africa]],omwe ali Angoni amene mfumu yawo inali [[Zwangendaba]]. Munthu woyambilira wa [[Chizungu]] amene anabwera ku Malawi anali [[David Livingstone]]. Iyeyu anafika ku [[chigwa]] cha kumpoto cha [[Nyanja ya Malawi]] mchaka cha [[1859]] ndipo ma [[tchalitchi]] a chi [[Sikotishi]] anatsatila m’mbuyo mwake kudzakhazikitsa ma tchalitchi. Boma la [[Britain]] linakhazikhitsa [[Nyasaland]] [[Protectorate]] mu chaka cha 1907. == Ndale == Dziko la [[Britain]] linalamulila mpaka chaka cha 1964, ngakhale anthu ena a Chimalawi anayeseysa kupeza ufulu wodzilamulira wokha. Mu zaka za m’ma 1950, nkhani yofuna ufulu wodzilamulira inakula, maka maka pamene dziko la Britain linakhazikitsa [[Chitaganya]] cha [[Rhodesia]] ndi [[Nyasaland]] mu chaka cha 1953. Mu 1958, [[Dokotala]] [[Hastings Kamuzu Banda]] anabwelera ku dzikoli atachokako kwa nthawi yaitali. Iyeyu anakhala mtsogoleli wa chipani cha [[Nyasaland African Congress]] chomwe pambuyo chinasinthidwa dzina kukhala [[Malawi Congress Party]] (MCP). Mu chaka cha 1959, Banda anamangidwa ndipo anatumizidwa ku [[Gweru]] [[Prison]] mu dziko la Southern Rhodesia (lomwe pano limatchedwa [[Zimbabwe]] chifukwa cha ndale zofuna kuti dzikoli lidzizilamulira lokha. Iyeyu anamasulidwa chaka cha 1960 pamene analoledwa kupita ku [[London]] mdziko la [[Britain]] kukatenga mbali pa msokhano wokambirana za malamulo. Pa 5 April 1961, [[chipani]] cha MCP chinapambana kuponsa zipani zonse pa chisankho chokhazikitsa ulamuliro wa tsopano. Ku msonkhano wokambirana za malamulo olamurira dziko ku London m’mwezi wa [[Novembala]] mu chaka cha 1962, boma la Britain linabvomera kuti Nyasaland likhale dziko lodzilamulira pa lokha. Chisankho chimenechi chinathetsa chitaganya cha Rhodesia ndi Nyasaland, chifukha dziko la Nyasaland likanakhala lodziimira pa lokha. Banda ansankhidwa kukhala [[Prime Minister]] pa 1 [[Febuluale]] 1963 ngakhale boma la Britain linkalamulirabe nkhani za chuma, chitetezo komanso ulamuliro wa dzikoli. Malamulo a tsopano olamulira dziko anakhazikitsidwa m’mwezi wa [[Meyi]] 1963, ndipo chitaganya chinathetsedwa pa 31 [[Disembala]] 1963. Dziko la Malawi linapatsidwa ufulu woyima pa lokha pa 6 [[Julaye]] 1964. Patapita zaka ziwili, dzikoli linakhala [[Lipabuliki]] lomwe [[Pulezidenti]] wake anali Dr. Banda ndipo analitchula kuti dziko lokhala ndi chipani chimodzi chokha. Mu 1970, Banda anapatsidwa u Pulezidenti wamuyaya wa MCP, ndipo 1971 anapatsidwa u Pulezidenti wa muyaya wa dziko la Malawi. Chifukwa cha kukula kwa kusakhutilitsidwa ndi ulamuliro wa Dr Banda, ndiponso makalata wolembedwa ndi mipingo ndiponso zonena za [[mabungwe osakhala a boma]], dziko la Malawi linapangitsa [[Referendamu]] yomwe anthu anafunsidwa boma lomwe iwo ankafuna. Pa 14 June 1993, anthu ochuluka a dzikoli anasankha kuti dzikoli likhale la zipani zambiri. Chisankho chinapangidwa pa 17 May 1994 ndipo [[Bakili Muluzi]] amene anali mtsogoleli wa [[United Democratic Front]] (UDF). Chipani cha UDF chinatenga mipando 82 mwa mipando 177 ya ku [[Nyumba yolamulira boma]] ndipo chinakhazikitsa mgwirizano ndi chipani cha [[Alliance For Democracy]] (AFORD). Mgwirizanowu unathetsedwa m’chaka cka 1966 koma ena mwa anthu amene anali a AFORD anatsalilabe m’mboma. [[Malamulo olamulira dziko]] amene anakhazikitsidwa mu 1995 anathetsa mphamvu zomwe zinali za chipani cha MCP. Kufulumizitsa [[kutsegula kwa malonda]] (economic libelarisation) ndi kukhonzatso kayendetsedwe ka zinthu m’dzikoli kunali mbali ya kusintha kwa ndale kwa dzikoli. Kusankhanso kwa Pulezidenti wina mu ulamuliro wa [[demokilase]] kunachitika mmwezi wa Meyi 2004 pamene woyimila UDF pa chisankhochi a [[Dr. Bingu wa Muntharika]] anapambana pa chisanko chomwe a [[John Tembo]] woyimira MCP ndi a [[Gwanda Chakuamba]] woyimira [[Mgwirizano Coalition]], limene linali gulu lomwe a mipingo ndi azipani zina ankatsatira. Chifukwa cha [[kampeni]] ndi dongosolo lomwe Bakili Muluzi anachita, chipani cha UDF chinankhazikitsa boma la zipani zambiri ndi zipani zina zotsutsa boma. [[File:Initiation ritual of boys in Malawi.jpg|thumb|250x250px]] == Maboma a Malawi == * Ku mpoto ** [[Chitipa]] ** [[Karonga]] ** [[Rumphi]] ** [[Mzuzu]] ** [[Mzimba]] ** ([[Ekwendeni]]) ** [[Nkhata Bay]] * Pakati ** '''[[Lilongwe]]''' (likulu) ** [[Dedza]] ** [[Ntcheu]] ** [[Kasungu]] ** [[Dowa]] ** ([[Mponela]]) ** [[Ntchisi]] ** [[Nkhotakota]] ** [[Salima]] * Kummwela ** [[Mangochi]] ** ([[Monkey Bay]]) ** [[Balaka]] ** [[Liwonde]] ** [[Machinga (mzinda)|Machinga]] ** [[Blantyre]] ** [[Zomba]] ** [[Chiradzulu]] ** [[Mulanje]] ** [[Phalombe]] ** [[Thyolo]] ** [[Mwanza]] ** [[Chikwawa]] ** [[Nsanje]] ** ([[Neno]]) <!-- ==Kumene kumapezeka dzikoli== ==Za Chuma== ==Za chikhalidwe cha anthu mdzikoli== ===Thanzi la anthu=== ===Nkhani ya chakudya=== ==Ubale ndi mayiko ena== ==Anthu amene amapezeka mdzikoli== ==Chikhalidwe cha anthu== ==Masamba ena onena za dzikoli== --> == Link == * [https://web.archive.org/web/20090318094611/http://www.humnet.ucla.edu/humnet/aflang/chichewa/chichewa.html#anchor125129 about Chichewa/Chinyanja] * [https://web.archive.org/web/20050307000211/http://www.sdnp.org.mw/webwshp/dkanjeza/ Mchoco University] [[Category:Malaŵi| ]] [[Category:Maiko a pa dziko lapansi]] [[Category:Maiko amene ankalamulidwa ndi dziko la Britain]] 5gn5t4ufdt5eoc26t154ym8m8xjw3id